Jeremiah 29:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akunena kuti, “Zitatha zaka makumi asanu ndi aŵiri ku Babiloni, ndidzakuyenderani ndi kuchitadi zimene ndidakulonjezani zija, ndipo ndidzakubwezerani ku malo ano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Yehova atero, kuti, Zitapita zaka makumi asanu ndi awiri pa Babiloni, ndidzakuyang'anirani inu, ndipo ndidzakuchitirani inu mau anga abwino, ndi kubwezera inu kumalo kuno.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, “Zaka 70 za ku Babuloni zikadzatha, ndidzabwera kudzakuchitirani zabwino zonse zimene ndinakulonjezani zija, ndipo ndidzakubwezerani ku malo ano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Yehova atero, kuti, Zitapita zaka makumi asanu ndi awiri pa Babulo, ndidzakuyang'anirani inu, ndipo ndidzakucitirani inu mau anga abwino, ndi kubwezera inu kumalo kuno.