Jeremiah 29:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzaŵapha ndi nkhondo, njala ndi mliri, ndipo ndidzaŵasandutsa chinthu chonyansa kwa anthu a maufumu onse a pa dziko lapansi. Adzakhala otembereredwa ndi ochititsa mantha, oŵaseka ndi onyozeka, pakati pa mitundu yonse ya anthu kumene ndidaŵapirikitsira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzatsata iwe ndi lupanga, ndi njala, ndi chaola, ndipo ndidzawapereka akhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko la pansi, akhale chitemberero, ndi chodabwitsa, ndi chotsonyetsa, ndi chitonzo, kwa mitundu yonse kumene ndinawapirikitsirako;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzawalondola ndi lupanga, njala ndi mliri ndipo ndidzawasandutsa chinthu chonyansa kwa anthu amayiko onse a pa dziko lapansi. Adzakhala otembereredwa, ochititsa mantha, onyozeka ndiponso ochitidwa chipongwe pakati pa anthu a mitundu yonse kumene ndawapirikitsirako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzatsata iwe ndi lupanga, ndi njala, ndi caola, ndipo ndidzawapereka akhale oopsyetsa m'maufumu onse a dziko la pansi, akhale citemberero, ndi codabwitsa, ndi cotsonyetsa, ndi citonzo, kwa mitundu yonse kumene ndinawapitikitsirako;