Jeremiah 29:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimenezi zidachitika pamene Yehoyakini ndi mfumukazi, nduna za mfumu ndi akuluakulu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu, ndiponso anthu aluso ndi osula, anali atachoka ku Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
anatero atachoka ku Yerusalemu Yekoniya mfumu ndi amake a mfumu ndi adindo ndi akulu a Yuda ndi a ku Yerusalemu, ndi amisiri, ndi achipala,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zimenezi zinachitika mfumu Yekoniya, amayi a mfumu, nduna za mfumu ndiponso atsogoleri a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu, anthu aluso ndi amisiri atatengedwa ku Yerusalemu kupita ku ukapolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
anatero atacoka ku Yerusalemu Yekoniya mfumu ndi amace a mfumu ndi adindo ndi akuru a Yuda ndi a ku Yerusalemu, ndi amisiri, ndi acipala,