Jeremiah 29:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Chauta Wamphamvuzonse wanenapo mau pa za Ahabu mwana wa Kalaya, ndi za Zedekiya mwana wa Maseiya, amene ankakuloserani zabodza m'dzina la Chautayo. Akuti, Ndidzaŵapereka kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, ndipo iyeyo adzaŵapha inu mukupenya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, za Ahabu mwana wake wa Koliya, ndi za Zedekiya mwana wake wa Maaseiya, amene anenera zonama m'dzina langa: Taonani, Ndidzawapereka m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni; ndipo iye adzawapha pamaso panu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti zokhudza Ahabu mwana wa Kolaya ndi Zedekiya mwana wa Maseya, amene akulosera zabodza kwa inu mʼdzina langa: “Taonani ndidzawapereka kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, ndipo adzawapha inu mukupenya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, za Ahabu mwana wace wa Koliya, ndi za Zedekiya mwana wace wa Maseya, amene anenera zonama m'dzina langa: Taonani, Ndidzawapereka m'dzanja la Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo; ndipo Iye adzawapha pamaso panu;