Jeremiah 29:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa cha anthu aŵiriwo, maina ao azidzaŵatchula anthu a ku Yuda okhala ku Babiloni potemberera anzao. Azidzati, ‘Chauta achite nawe monga m'mene adachitira ndi Zedekiya ndi Ahabu amene mfumu ya ku Babiloni adaŵatentha!’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo am'nsinga onse a Yuda amene ali m'Babiloni adzatemberera pali iwo, kuti, Yehova akuchitire iwe monga Zedekiya ndi Ahabu, amene mfumu ya ku Babiloni inaocha m'moto;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa cha anthu awiriwo, akapolo onse ochokera ku Yuda amene ali ku Babuloni adzagwiritsa ntchito mawu awa potemberera: ‘Yehova achite nawe monga mmene anachitira ndi Zedekiya ndi Ahabu, amene mfumu ya ku Babuloni inawatentha.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo am'nsinga onse a Yuda amene ali m'Babulo adzatemberera pali iwo, kuti, Yehova akucitire iwe monga Zedekiya ndi Ahabu, amene mfumu ya ku Babulo inaoca m'moto;