Jeremiah 29:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zoonadi makhalidwe ao ku Israele analidi oipa, ankachita chigololo ndi akazi a eniake, ankalosa zabodza m'dzina langa, Ine osaŵalamula. Ine ndikuzidziŵa, ndingathe kuzichitira umboni zimenezi,” akuterotu Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa anachita zopusa m'Israele, nachita chigololo ndi akazi a anansi ao, nanena mau onama m'dzina langa, amene ndinawauza kuti asanene; Ine ndine wodziwa, ndi mboni, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti anthu amenewa achita zoyipa kwambiri mu Israeli; achita chigololo ndi akazi a eni ake ndipo mʼdzina langa ankayankhula zabodza zimene sindinawawuze kuti atero. Ine ndikuzidziwa ndipo ndine mboni ya zimenezi,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa anacita zopusa m'Israyeli, nacita cigololo ndi akazi a anansi ao, nanena mau onama m'dzina langa, amene ndinawauza kuti asanene; Ine ndine wodziwa, ndi mboni, ati Yehova.