Jeremiah 29:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mau a Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, ndi aŵa akuti: Iweyo udatumiza kalata m'dzina lako kwa anthu onse a ku Yerusalemu, kwa Zefaniya wansembe mwana wa Maseiya, ndi kwa ansembe onse. M'kalatamo udanena kuti
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, kuti, Chifukwa watumiza akalata m'dzina lako iwe mwini kwa anthu onse amene akhala ku Yerusalemu, ndi kwa Zefaniya mwana wake wa Maaseiya wansembe, ndi kwa ansembe onse, kuti,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Iwe unatumiza kalata mʼdzina lako kwa anthu onse a mu Yerusalemu, kwa Zefaniya mwana wa wansembe Maseya, ndi kwa ansembe onse. Unalemba mu kalatayo kuti,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, kuti, Cifukwa watumiza akalata m'dzina lako iwe mwini kwa anthu onse amene akhala ku Yerusalemu, ndi kwa Zefaniya mwana wace wa Maseya wansembe, ndi kwa ansembe onse, kuti.