Jeremiah 29:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta wakuika iwe Zefaniya, kuti ukhale wansembe m'malo mwa wansembe Yehoyada. Wakuika kuti ukhale kapitao woyang'anira Nyumba ya Chauta. Uzimponya m'ndende ndi kumuveka goli munthu aliyense wamsala amene amadziyesa mneneri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova anakuyesa iwe wansembe m'malo mwa Yehoyada wansembe, kuti iwe ndi anzako mudzakhale akapitao m'nyumba ya Yehova, oyang'anira munthu yense wamisala, wodziyesa mneneri, kuti umuike iye m'zigologolo ndi m'goli.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
‘Yehova wakusankha kukhala wansembe mʼmalo mwa Yehoyada kuti ukhale wamkulu woyangʼanira Nyumba ya Yehova. Munthu aliyense wamisala amene akudziyesa kuti ndi mneneri uzimuponya mʼndende ndi kumuveka goli lachitsulo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova anakuyesa iwe wansembe m'malo mwa Yehoyada wansembe, kuti iwe ndi anzako mudzakhale akapitao m'nyumba ya Yehova, oyang'anira munthu yense wamisala, wodziyesa mneneri, kuti umuike iye m'zigologolo ndi m'gori.