Jeremiah 29:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ifetu ku Babiloni kuno Yeremiyayo watitumizira mau akuti: Ukapolo wanu ukhala wautali. Mangani nyumba zoti muzikhalamo, ndipo limani minda kuti muzidya zipatso zake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
popeza watitumizira mau ku Babiloni, akuti, Undende udzakhalitsa; mangani nyumba, khalani m'menemo; limani minda, idyani zipatso zao?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yeremiyayo watitumizira uthenga uwu kuno ku Babuloni: Ukapolo wanu ukhala wa nthawi yayitali. Choncho mangani nyumba ndipo muzikhalamo; limani minda ndipo mudye zipatso zake.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
popeza watitumizira mau ku Babulo, akuti, Undende udzakhalitsa; mangani nyumba, khalani m'menemo; limani minda, idyani zipatso zao?