Jeremiah 29:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yeremiya kalatayo adapatsira Elasa mwana wa Safani, ndi Gemariya mwana wa Hilikiya, amene Zedekiya mfumu ya ku Yuda adaaŵatuma ku Babiloni kwa mfumu Nebukadinezara. M'kalatamo adaalembamo kuti,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
anatumiza kalatayo m'dzanja la Elasa mwana wake wa Safani, ndi Gemariya mwana wake wa Hilikiya, amene Zedekiya mfumu ya Yuda anawatuma ku Babiloni kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, kuti,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yeremiya anapatsira kalatayo Eleasa mwana wa Safani ndi Gemariya mwana wa Hilikiya, amene Zedekiya mfumu ya Yuda anawatumiza kwa Mfumu Nebukadinezara ku Babuloni. Mʼkalatamo analembamo kuti:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
anatumiza kalatayo m'dzanja la Elasa mwana wace wa Safani, ndi Gemariya mwana wace wa Hilikiya, amene Zedekiya mfumu ya Yuda anawatuma ku Babulo kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo, kuti,