Jeremiah 29:32 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake Ine Chauta ndikunena kuti: Ndidzamlanga Semaya pamodzi ndi zidzukulu zake. M'banja lakelo palibe munthu amene adzakhale pakati pa mtundu uno wa anthu, amene adzaone zabwino zomwe ndidzachitira anthu anga, chifukwa iyeyo walalika zondipandukira,” akuterotu Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa chake atero Yehova, Taonani, ndidzalanga Semaya Mnehelamu, ndi mbeu zake; sadzakhala ndi munthu wakukhala mwa anthu awa, sadzaona zabwino ndidzachitira anthu anga, ati Yehova: chifukwa wanena zopikisana ndi Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake Ine Yehova ndikuti: Mʼbanja lakelo sipadzakhala munthu pakati pa mtundu uno wa anthu amene adzaone zinthu zabwino zimene ndidzachitira anthu anga chifukwa analalika zondiwukira,’ ” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa cace atero Yehova, Taonani, ndidzalanga Semaya Mnehelamu, ndi mbeu zace; sadzakhala ndi munthu wakukhala mwa anthu awa, sadzaona za bwino ndidzacitira anthu anga, ati Yehova: cifukwa wanena zopikisana ndi Yehova.