Jeremiah 29:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukwatire, ndipo mubale ana aamuna ndi ana aakazi. Ana aamunawo muŵasankhire akazi, ana aakaziwo muŵasankhire amuna, kuti abale ana aamuna ndi ana aakazi. Ndipo muchulukane kumeneko, osachepa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
tengani akazi, balani ana aamuna ndi aakazi; kwatitsani ana anu amuna, patsani ananu akazi kwa amuna, kuti abale ana aamuna ndi aakazi; kuti mubalane pamenepo musachepe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwatirani ndipo mubereke ana aamuna ndi aakazi. Ana anu aamuna muwasankhire akazi ndipo muwasankhire amuna ana anu aakaziwo, kuti nawonso abale ana aamuna ndi aakazi. Muchulukane kumeneko. Chiwerengero chanu chisachepe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
tengani akazi, balani ana amuna ndi akazi; kwatitsani ana anu amuna, patsani ananu akazi kwa amuna, kuti abale ana amuna ndi akazi; kuti mubalane pamenepo, musacepe.