Jeremiah 29:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muzikometsa ku mizinda kumene ndidakupirikitsirani ku ukapoloko, kuti zonse zizikuyenderani bwino. Muzipempherera mizindayo kwa Chauta, chifukwa choti mizindayo ikakhala pa mtendere, inunso mudzakhala pabwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nimufune mtendere wa mudzi umene ndinakutengerani am'nsinga, nimuwapempherere kwa Yehova; pakuti mwa mtendere wake inunso mudzakhala ndi mtendere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndiponso muzifunafuna mtendere ndi ubwino wa mzinda umene ndinakupirikitsirani ku ukapoloko. Muzipempherera mzindawo kwa Yehova, kuti zikuyendereni bwino.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nimufune mtendere wa mudzi umene ndinakutengerani am'nsinga, nimuwapempherere kwa Yehova; pakuti mwa mtendere wace inunso mudzakhala ndi mtendere.