Jeremiah 3:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pita ukalalike kumpoto uthenga uwu wakuti, “ ‘Israele wosakhulupirikawe, bwerera,’ akuterotu Chauta. ‘Ukali wanga sudzapitirira, poti ndine wachifundo. Sindidzakukwiyira mpaka muyaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pita; nulalikire mau awa kuyang'ana kumpoto, ndi kuti, Bwera iwe Israele wobwerera, ati Yehova; sindidzakuyang'anira iwe ndi kukwiya; pakuti Ine ndili wachifundo, ati Yehova, sindidzakhala nako kukwiya kunthawi zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pita ukalalikire kumpoto uthenga wakuti, “ ‘Israeli wosakhulupirikawe, bwerera,’ akutero Yehova. ‘Sindidzakukalipira mpaka kalekale, pakuti ndine wachifundo,’ akutero Yehova. ‘Sindidzakukwiyira mpaka kalekale.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pita; nulalikire mau awa kuyang'ana kumpoto, ndi kuti, Bwera iwe Israyeli wobwerera, ati Yehova; sindidzakuyang'anira iwe ndi kukwiya; pakuti Ine ndiri wacifundo, ati Yehova, sindidzakhala nako kukwiya ku nthawi zonse.