Jeremiah 3:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Bwererani inu anthu osakhulupirika, pakuti mbuye wanu ndine. Ndidzakutengani kupita nanu ku Ziyoni, mmodzi kuchokera ku mzinda uliwonse, aŵiri kuchokera ku banja lililonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Bwerani, ananu obwerera, ati Yehova; pakuti Ine ndine mbuye wanu; ndipo ndidzakutengani inu mmodzimmodzi wa pa mudzi uliwonse, ndi awiriawiri a pa banja lililonse, ndi kukutengerani ku Ziyoni;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Bwererani, ana osakhulupirika, pakuti ndine mbuye wanu,” akutero Yehova. “Ndinakusankhani, mmodzimmodzi kuchokera ku mudzi uliwonse ndiponso awiriawiri kuchokera ku banja lililonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Bwerani, ananu obwerera, ati Yehova; pakuti Ine ndine mbuye wanu; ndipo ndidzakutengani inu mmodzi mmodzi wa pa mudzi uli wonse, ndi awiri awiri a pa banja liri lonse, ndi kukutengerani ku Ziyoni;