Jeremiah 3:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Masiku amenewo mukadzachulukana m'dzikomo, anthu sadzalankhulanso za bokosi lachipangano la Chauta. Sadzaliganizira kapena kulikumbukira kapena kulisoŵa, ndipo sadzapanganso lina.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo padzaoneka, pamene mudzakhala ambiri ndi kuchuluka m'dzikomo masiku awo, ati Yehova, sadzatinso konse, Likasa la chipangano cha Yehova; silidzalowa m'mtima; sadzalikumbukira; sadzanka kukaliona, sadzachitanso konse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Masiku amenewo mukadzachulukana kwambiri mʼdzikomo, anthu sadzanenanso za ‘Bokosi la Chipangano la Yehova’ kapena kuliganizira. Sadzalikumbukiranso kapena kulifuna, ndipo sadzapanganso lina,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo padzaoneka, pamene mudzakhala ambiri ndi kucuruka m'dzikomo masiku awo, ati Yehova, sadzatinso konse, Likasa la cipangano ca Yehova; silidzalowa m'mtima; sadzalikumbukira; sadzanka kukaliona, sadzacitanso konse.