Jeremiah 3:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Masiku amenewo fuko la Yuda lidzaphathana ndi fuko la Israele. Onse pamodzi adzachokera ku dziko lakumpoto kupita ku dziko limene ndidapatsa makolo ao, kuti likhale choloŵa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Masiku omwewo nyumba ya Yuda idzayenderena ndi nyumba ya Israele, ndipo adzatuluka pamodzi kudziko la kumpoto kunka ku dziko limene ndinapatsa makolo anu kuti alowemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Masiku amenewo fuko la Yuda lidzaphatikizana ndi fuko la Israeli, onse pamodzi adzachokera ku dziko la kumpoto kupita ku dziko limene ndinapatsa makolo awo, kuti likhale cholowa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Masiku omwewo nyumba ya Yuda idzayenderana ndi nyumba ya Israyeli, ndipo adzaturuka pamodzi ku dziko la kumpoto kunka ku dziko limene ndinapatsa makolo anu kuti alowemo.