Jeremiah 3:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akunena kuti, “Iwe Israele, ndikadakonda kukukhazika pakati pa ana anga, ndi kukupatsa dziko lokoma, choloŵa chokongola kwambiri kupambana maiko a mitundu ina ya anthu. Ndidaganiza kuti udzanditchula ‘Atate’, ndipo kuti sudzaleka kumanditsata.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Ine ndinati, Ndidzakuika iwe bwanji mwa ana, ndi kupatsa iwe dziko lokondweretsa, cholowa chabwino cha makamu a mitundu ya anthu? Ndipo ndinati mudzanditcha Ine, Atate wanga; osatembenuka kuleka kunditsata Ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ine mwini ndinati, “ ‘Ndikanakonda bwanji kukukhazikani pakati pa ana anga ndikukupatsani dziko labwino kwambiri, cholowa chokongola kwambiri kuposa cha mitundu ina ya anthu.’ Ndinaganiza kuti mudzanditcha Ine ‘Atate’ ndi kuti simudzaleka kunditsata.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Ine ndinati, Ndidzakuika iwe bwanji mwa ana, ndi kupatsa iwe dziko lokondweretsa, colowa cabwino ca makamu a mitundu ya anthu? ndipo ndinati mudzandicha Ine, Atate wanga; osatembenuka kuleka kunditsata Ine.