Jeremiah 3:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Uyang'ane ku zitunda zonse zachipembedzo. Mpoti pamene sudachitepo zadama? Unkakhala m'mbali mwa njira kumadikirira zibwenzi zako, ngati Mluya wobisalira anthu m'chipululu. Waipitsa dziko ndi mkhalidwe wako woipa wachiwerewere.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwezera maso ako kumapiri oti see, nuone: sanagona ndi iwe kuti? Panjira wakhalira iwo, monga Mwarabu m'chipululu; ndipo waipitsa dziko ndi zigololo zako, ndi zoipa zako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tayangʼana ku zitunda zowuma. Kodi aliponso malo ena amene iwe sunachitepo zadama? Iwe unkakhala mʼmbali mwa njira kumadikira zibwenzi zako, ngati Mluya wobisalira anthu mʼchipululu. Inu mwayipitsa dziko ndi zadama zanu ndi ntchito zanu zoyipa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kwezera maso ako ku mapiri oti se, nuone: sanagona ndi iwe kuti? Panjira wakhalira iwo, monga M-arabu m'cipululu; ndipo waipitsa dziko ndi zigololo zako, ndi zoipa zako.