Jeremiah 3:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kupembedza pa magomo sikuthandiza, kuchita maphwando pa mapiri kulibenso ntchito. Zoonadi, mwa Chauta, Mulungu wathu ndiye muli chipulumutso cha Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndithu akhulupirira mwachabe chithandizo cha kuzitunda, ndi phokoso la kumapiri; ndithu mwa Yehova Mulungu wathu muli chipulumutso cha Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndithu kupembedza pa magomo komanso kuchita maphwando pa mapiri zilibe phindu. Zoonadi chipulumutso cha Israeli chili mwa Yehova Mulungu wathu basi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndithu akhulupirira mwacabe cithandizo ca kuzitunda, ndi phokoso la kumapiri; ndithu mwa Yehova Mulungu wathu muli cipulumutso ca Israyeli,