Jeremiah 3:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Kuchokera pa chiyambi cha mtundu wathu, Baala, mulungu wochititsa manyazi uja, wakhala akutiwonongetsa phindu la ntchito ya makolo athu, ndiye kuti nkhosa ndi ng'ombe zao, ana ao aamuna ndi ana ao aakazi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chochititsa manyazi chinathetsa ntchito za atate athu kuyambira ubwana wathu; nkhosa zao ndi zoweta zao, ana ao aamuna ndi aakazi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuyambira pa ubwana wathu milungu yochititsa manyazi ija yakhala ikutiwonongetsa phindu la ntchito za makolo athu, nkhosa ndi ngʼombe zawo, ana awo aamuna ndi aakazi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo cocititsa manyazi cinathetsa nchito za atate athu kuyambira ubwana wathu; nkhosa zao ndi zoweta zao, ana ao amuna ndi akazi.