Jeremiah 3:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono tigone pansi mwamanyazi, ndipo kunyozeka kwathu kutiphimbe. Paja tidachimwa ife pamodzi ndi makolo athu, kuchimwira Chauta Mulungu wathu, kuyambira ubwana wathu mpaka lero lino. Sitidamvere mau a Chauta Mulungu wathu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tigone m'manyazi athu, kunyala kwathu kutifunde ife; pakuti tamchimwira Yehova Mulungu wathu, ife ndi makolo athu, kuyambira ubwana wathu kufikira lero lomwe; ndipo sitidamvera mau a Yehova Mulungu wathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tilekeni tigone pansi mwa manyazi, ndipo kunyozeka kwathu kutiphimbe. Paja tachimwira Yehova Mulungu wathu, ife pamodzi ndi makolo athu kuyambira nthawi ya ubwana wathu mpaka lero lino sitinamvere Yehova Mulungu wathu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tigone m'manyazi athu, kunyala kwathu kutipfunde ife; pakuti tamcimwira Yehova Mulungu wathu, ife ndi makolo athu, kuyambira ubwana wathu kufikira lero lomwe; ndipo sitidamvera mau a Yehova Mulunguwathu.