Jeremiah 3:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
‘Kodi Chauta adzandipsera mtima nthaŵi zonse? Kodi adzakwiya mpaka muyaya?’ Umu ndimo m'mene unkalankhulira. Komabe iwe udapitiriza kuchita zoipa monga momwe unkathera.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi adzasunga mkwiyo wake kunthawi zonse? Kodi adzakudikira mpaka chimaliziro? Taona, wanena ndi kuchita zoipa monga unatero.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
kodi mudzandikwiyira nthawi zonse? Kodi ukali wanu udzakhalabe mpaka muyaya?’ Umu ndimo mmene umayankhulira, koma umapitirizabe kuchita zoyipa monga momwe umathera.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi adzasunga mkwiyo wace ku nthawi zonse? Kodi adzakudikira mpaka cimariziro? Taona, wanena ndi kucita zoipa monga unatero.