Jeremiah 3:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa nthaŵi ya mfumu Yosiya, Chauta adati, “Kodi waona zimene wosakhulupirika uja Israele adachita? Ankakwera kukapembedza pa phiri, ndi patsinde pa mtengo uliwonse wogudira. Motero kumeneko ankakachita zadama.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa ine masiku a Yosiya mfumu, Kodi waona chimene wachichita Israele, wobwerera m'mbuyo? Wakwera pa mapiri atali onse, ndi patsinde pa mitengo yaiwisi yonse, ndi kuchita dama pamenepo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawi ya Mfumu Yosiya Yehova anandiwuza kuti, “Kodi waona zomwe Israeli wosakhulupirika uja wachita? Anakwera pa phiri lililonse lalitali ndi kupita pa tsinde pa mtengo uliwonse wogudira kukapembedza. Choncho anachita za chiwerewere kumeneko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa ine masiku a Yosiya mfumu, Kodi waona cimene wacicita Israyeli, wobwerera m'mbuyo? Wakwera pa mapiri atari onse, ndi patsinde pa mitengo yaiwisi yonse, ndi kucita dama pamenepo.