Jeremiah 30:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine ndili nanu, ndipo ndidzakupulumutsani,” akuterotu Chauta. “Ndidzaononga mitundu yonse ya anthu kumene ndidakubalalitsani, koma inu sindidzakuwonongani kotheratu. Ndidzakulangani potsata chilungamo, sindingakulekerereni osakulangani konse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Ine ndili ndi iwe, ati Yehova, kuti ndipulumutse iwe; koma ndidzatha ndithu amitundu onse amene ndinakumwazira mwa iwo, koma sindidzatha iwe ndithu; koma ndidzakulangiza iwe ndi chiweruziro, ndipo sindidzakuyesa wosapalamula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndili nanu ndipo ndidzakupulumutsani,’ akutero Yehova. ‘Ngakhale ndidzawononga kotheratu mitundu yonse ya anthu kumene ndinakubalalitsirani, koma inu sindidzakuwonongani kotheratu. Sindidzakulekani kuti mukhale osalangidwa. Koma ndidzakulangani mwachilungamo.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Ine ndiri ndi iwe, ati Yehova, kuti ndipulumutse iwe; koma ndidzatha ndithu amitundu onse amene ndinakumwazira mwa iwo, koma sindidzatha iwe ndithu; koma ndidzakulangiza iwe ndi ciweruziro, ndipo sindidzakuyesa wosaparamula.