Jeremiah 30:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abwenzi anu onse akuiŵalani, sakulabadiraninso. Ndakulangani mwankhanza, poti mlandu wanu ndi waukulu, machimo anu ndi ambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mabwenzi ako onse anakuiwala iwe; salikukufuna iwe; pakuti ndakulasa ndi bala la mdani, ndi kulanga kwa wankhanza; chifukwa cha mphulupulu yako yaikulu, chifukwa zochimwa zako zinachuluka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abwenzi anu onse akuyiwalani; sasamalanso za inu. Ndakukanthani ngati mmene mdani akanachitira. Ndipo ndakulangani mwa nkhanza, chifukwa machimo anu ndi ambiri, ndipo kulakwa kwanu ndi kwakukulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mabwenzi ako onse anakuiwala iwe; salikukufuna iwe; pakuti ndakulasa ndi bala la mdani, ndi kulanga kwa wankhanza; cifukwa ca mphulupulu yako yaikuru, cifukwa zocimwa zako zinacuruka.