Jeremiah 30:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa chiyani mukudandaula nacho chilonda chanu? Bala lanu silingapole ai. Mlandu wanu ndi waukulu, machimo anu ngambiri, nchifukwa chake ndakuchitani zimenezi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chanji ulirira bala lako? Kuphwetekwa kwako kuli kosapoleka; chifukwa cha mphulupulu yako yaikulu, chifukwa zochimwa zako zinachuluka, ndakuchitira iwe izi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa chiyani mukulira nacho chilonda chanu? Bala lanu silingapole ayi. Ine ndakuchitani zimenezi chifukwa machimo anu ndi ambiri ndipo kulakwa kwanu nʼkwakukulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa canji ulilira bala lako? kuphwetekwa kwako kuli kosapoleka; cifukwa ca mphulupulu yako yaikuru, cifukwa zocimwa zako zinacuruka, ndakucitira iwe izi.