Jeremiah 30:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono onse amene adakuwonongani inu, ndidzaŵaononga iwonso. Onse okuzunzani adzatengedwa ukapolo. Onse ofunkha zinthu zanu, nawonso zao zidzafunkhidwa. Ndipo onse okusakazani, ndidzachita zoti nawonso aŵasakaze.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake iwo akulusira iwe adzalusidwanso; ndi adani ako onse, adzanka ku undende onsewo; ndipo iwo adzakufunkha iwe adzakhala chofunkha, ndipo onse akulanda iwe ndidzapereka kuti zilandidwe zao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsono onse amene anakuwonongani, nawonso adzawonongedwa; adani anu onse adzapita ku ukapolo. Iwo amene anafunkha zinthu zanu, zinthu zawo zidzafunkhidwanso; onse amene anakusakazani nawonso adzasakazidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace iwo akulusira iwe adzalusidwanso; ndi adani ako onse, adzanka kuundende onsewo; ndipo iwo adzakufunkha iwe adzakhala cofunkha, ndipo onse akulanda iwe ndidzapereka kuti zilandidwe zao.