Jeremiah 30:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma inuyo, ndidzachiza matenda anu, ndidzapoletsa mabala anu, chifukwa anthu ena amati ndinu otayika, amati, ‘Ndi anthu a ku Ziyoni aŵa, opanda oŵasamala,’ ” akuterotu Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndidzakubwezera iwe moyo, ndipo ndidzapoletsa mabala ako, ati Yehova; chifukwa anatcha iwe wopirikitsidwa, nati, Ndiye Ziyoni, amene kulibe munthu amfuna.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzachiza matenda anu ndi kupoletsa zilonda zanu, akutero Yehova, ‘chifukwa mukutchedwa anthu otayika. Amati, ndi anthu a ku Ziyoni awa amene alibe wowasamala.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndidzakubwezera iwe moyo, ndipo ndidzapoletsa mabala ako, ati Yehova; cifukwa anacha iwe wopitikitsidwa, nati, Ndiye Ziyoni, amene kulibe munthu amfuna.