Jeremiah 30:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akunena kuti, “Ndidzabwezeranso a banja la Yakobe ku dziko lao. Ndidzaonetsanso chikondi changa ku malo ake onse. Mzinda wa Yerusalemu uja udzamangidwanso pabwinja pake pompaja. Nyumba yaufumu idzamangidwanso pamalo pake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova: Taonani, ndidzabwezanso undende wa mahema a Yakobo, ndipo ndidzachitira chifundo zokhalamo zake, ndipo mudzi udzamangidwa pamuunda pake, ndi chinyumba chidzakhala momwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, “Ndidzabwera nalo banja la Yakobo ku dziko lawo ndipo ndidzachitira chifundo malo ake okhalamo; mzinda wa Yerusalemu udzamangidwanso pa bwinja pake, nyumba yaufumu idzamangidwanso pa malo pake penipeni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova: Taonani, ndidzabwezanso undende wa mahema a Yakobo, ndipo ndidzacitira cifundo zokhalamo zace, ndipo mudzi udzamangidwa pamuunda pace, ndi cinyumba cidzakhala momwe.