Jeremiah 30:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wodzaŵalamulira adzakhala mmodzi mwa iwo. Mtsogoleri wao adzachokera pakati pao. Ineyo ndidzamkokera pafupi nane, ndipo iye adzayandikana nane. Ndanitu angalimbe mtima payekha kuti ayandikane ndi Ine?” Akutero Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mkulu wao adzakhala mwa iwo, ndi wolamulira wao adzatuluka pakati pao; ndipo ndidzamyandikitsa iye, ndipo adzayandikira kwa Ine, pakuti iye wolimba mtima kuyandikira kwa Ine ndani? Ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mtsogoleri wawo adzakhala mmodzi mwa iwo. Wodzawalamulira adzachokera pakati pawo. Choncho ndidzawakokera kufupi ndi Ine ndipo iye adzandiyandikira. Ndani angalimbe mtima payekha kuyandikana nane popanda kuyitanidwa?” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mkuru wao adzakhala mwa iwo, ndi wolamulira wao adzaturuka pakati pao; ndipo ndidzamyandikitsa iye, ndipo adzayandikira kwa Ine, pakuti iye wolimba mtima kuyandikira kwa Ine ndani? ati Yehova.