Jeremiah 30:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kalanga ine! Tsiku limenelo nlalikulu kwambiri, sipadzakhala lina lofanana nalo. Idzakhala nthaŵi yamavuto kwa Yakobe, komabe adzapulumuka ku mavutowo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kalanga ine! Pakuti nlalikulu tsikulo, palibe lina lotere; ndi nthawi ya msauko wa Yakobo; koma adzapulumuka m'menemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mayo ine! Tsiku limeneli ndi lalikulu kwambiri! Sipadzakhala lina lofanana nalo. Idzakhala nthawi ya masautso kwa Yakobo, koma adzapulumuka ku masautsowo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kalanga ine! pakuti nlalikuru tsikulo, palibe lina lotere; ndi nthawi ya msauko wa Yakobo; koma adzapulumuka m'menemo.