Jeremiah 31:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthuwo adzabwera akuimba mofuula pa mapiri a Ziyoni, adzakhala osangalala kwambiri chifukwa cha zabwino zochuluka zochokera kwa Chauta. Zabwinozo ndi izi: tirigu, vinyo watsopano, mafuta, anaankhosa ndi anaang'ombe. Moyo wao udzakhala ngati munda wothirira, ndipo sadzamvanso chisoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo adzadza nadzaimba pa msanje wa Ziyoni, nadzasonkhanira ku zokoma za Yehova, kutirigu, ndi kuvinyo, ndi mafuta, ndi kwa ana a zoweta zazing'ono ndi zazikulu; ndipo moyo wao udzakhala ngati munda wamichera; ndipo sadzakhalanso konse ndi chisoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthuwo adzabwera akuyimba mofuwula pa mapiri a Ziyoni; adzasangalala ndi zinthu zabwino zochokera kwa Yehova. Zinthu zabwinozo ndi izi: tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta, ana ankhosa ndi ana angʼombe. Iwo adzakhala ngati munda wothiriridwa bwino, ndipo sadzamvanso chisoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo adzadza nadzayimba pa msanje wa Ziyoni, nadzasonkhanira, ku zokoma za Yehova, kutirigu, ndi kuvinyo, ndi mafuta, ndi kwa ana a zoweta zazing'ono ndi zazikuru; ndipo moyo wao udzakhala ngati munda wamicera; ndipo, sadzakhalanso konse ndi cisoni.