Jeremiah 31:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mau a Chauta ndi aŵa: “Imvani, kulira kukumveka ku Rama, kulira komvetsa chisoni. Rakele akulira ana ake. Sakutonthozeka, chifukwa choti ana ake asoŵa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova: Mau a amveka m'Rama, maliro ndi kulira kwakuwawa, Rakele alinkulirira ana ake; akana kutonthozedwa mtima pa ana ake, chifukwa palibe iwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, “Kulira kukumveka ku Rama, kulira kwakukulu, Rakele akulirira ana ake. Sakutonthozeka chifukwa ana akewo palibe.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova: Mau amveka m'Rama, maliro ndi kulira kwakuwawa, Rakeli alinkulirira ana ace; akana kutonthozedwa mtima pa ana ace, cifukwa palibe iwo.