Jeremiah 31:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akunena kuti, “Tonthola, usadzenso misozi. Ndithu udzalandira mphotho ya ntchito zako, akutero Chauta. Ndipo anthu adzabwerako ku dziko la adani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova atero: Letsa mau ako asalire, ndi maso anu asagwe misozi; pakuti ntchito yako idzalandira mphotho, ati Yehova; ndipo adzabweranso kuchokera kudziko la mdani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, “Leka kulira ndi kukhetsa misozi pakuti udzalandira mphotho ya ntchito yako,” akutero Yehova. “Iwo adzabwerako ku dziko la adani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova atero: Letsa mau ako asalire, ndi maso anu asagwe misozi; pakuti nchito yako idzalandira mphoto, ati Yehova; ndipo adzabweranso kucokera ku dziko la mdani.