Jeremiah 31:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndamva Aefuremu akulira mwachisoni kuti, ‘Inu mwatilanga ngati mwanawang'ombe wosaphunzitsidwa, ndipo taphunziradi kumvera. Mutibweze kuti tithe kubwerera, Pakuti inu ndinu Chauta, Mulungu wathu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kumva ndamva Efuremu alinkulirira kotero, Mwandilanga ine, ndipo ndalangidwa, monga mwanawang'ombe wosazolowera goli; munditembenuze ine, ndipo ine ndidzatembenuka; pakuti inu ndinu Yehova Mulungu wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndithu ndamva Efereimu akubuwula kuti, ‘Ife tinali ngati ana angʼombe osamva. Koma inu mwatiphunzitsa kumvera. Mutibweze kuti tithe kubwerera, chifukwa ndinu Yehova Mulungu wanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kumva ndamva Efraimu alinkulirira kotero, Mwandilanga ine, ndipo ndalangidwa, monga mwana wa ng'ombe wosazolowera gori; munditembenuze ine, ndipo ine ndidzatembenuka; pakuti inu ndinu Yehova Mulungu wanga.