Jeremiah 31:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsopano poti tatembenuka mtima, tikumva chisoni. Tsopano poti taphunzira, tikudzigunda pa mtima. Tachita manyazi ndipo tanyazitsidwa, chifukwa cha machimo athu apaubwana.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti nditatembenuka, ndinalapa; nditalangizidwa, ndinamenya pa ntchafu yanga; ndinakhala ndi manyazi, inde, ndinapepulidwa, chifukwa ndinasenza chitonzo cha ubwana wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Popeza tatembenuka mtima, ndiye tikumva chisoni; popeza tazindikira ndiye tikudziguguda pachifukwa. Tachita manyazi ndipo tanyazitsidwa chifukwa tinachimwa paubwana wathu.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti nditatembenuka, ndinalapa; nditalangizidwa, ndinamenya pa ncafu yanga; ndinakhala ndi manyazi, inde, ndinapepulidwa, cifukwa ndinasenza citonzo ca ubwana wanga.