Jeremiah 31:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi suja Efuremu ndi mwana wanga wapamtima, mwana amene ndimakondwera naye kwambiri? Nthaŵi zonse ndikamamdzudzula, ndimamkumbukirabe ndi chikondi, mwakuti mtima wanga umamlakalaka. Ndimamumvera chifundo chozama zedi,” akuterotu Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi Efuremu ndiye mwana wanga wokondedwa? Kodi ndiye mwana wokondweretsa? Nthawi zonse zoti ndimnenera zomtsutsa, pakuti ndimkumbukiranso ndithu; chifukwa chake mumtima mwanga ndimlirira; ndidzamchitiradi chifundo, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi Efereimu si mwana wanga wokondedwa, mwana amene Ine ndimakondwera naye? Ngakhale nthawi zambiri ndimamudzudzula, ndimamukumbukirabe. Kotero mtima wanga ukumufunabe; ndimamumvera chifundo chachikulu kwambiri,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi Efraimu ndiye mwana wanga wokondedwa? Kodi ndiye mwana wokondweretsa? nthawi zonse zoti ndimnenera zomtsutsa, pakuti ndimkumbukiranso ndithu; cifukwa cace mumtima mwanga ndimlirira; ndidzamcitiradi cifundo, ati Yehova.