Jeremiah 31:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi udzakhala ukutepeka mpaka liti, iwe mwana wanga wosakhulupirika? Zoona, Chauta walenga chinthu chatsopano pa dziko lapansi: mkazi ndiye atsogola kufunafuna mwamuna.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Udzayenda kwina ndi kwina masiku angati, iwe mwana wamkazi wobwerera m'mbuyo? Pakuti Yehova walenga chatsopano m'dziko lapansi: mkazi adzasanduka mphongo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Udzakhala jenkha mpaka liti, iwe mwana wa mkazi wosakhulupirika? Yehova walenga chinthu chatsopano pa dziko lapansi; mkazi ndiye tsopano aziteteza mwamuna.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Udzayenda kwina ndi kwina masiku angati; iwe mwana wamkazi wobwerera m'mbuyo? pakuti Yehova walenga catsopano m'dziko lapansi: mkazi adzasanduka mphongo.