Jeremiah 31:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, “Pamene ndidzabwezeranso anthu ufulu, kudzamvekanso mau ku dziko la Yuda ndi ku mizinda yake. Mau ake adzakhala akuti, ‘Chauta akudalitse iwe malo achilungamo, ndiponso iwe phiri loyera.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Kawirinso adzanena mau awa m'dziko la Yuda ndi m'midzi yake, pamene ndibwezanso undende wao; Yehova akudalitse iwe, wokhalamo chilungamo, iwe phiri lopatulika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, “Ndikadzabwera nawo anthuwa kuchokera ku ukapolo, anthu a mʼdziko la Yuda ndi amene akukhala mʼmizinda yake adzayankhulanso mawu akuti, ‘Yehova akudalitse, iwe malo achilungamo, iwe phiri lopatulika.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, Kawirinso adzanena mau awa m'dziko la Yuda ndi m'midzi yace, pamene ndibwezanso undende wao; Yehova akudalitse iwe, wokhalamo cilungamo, iwe phiri lopatulika.