Jeremiah 31:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sichidzakhalanso ngati chipangano chija chimene ndidaachita ndi makolo ao, pamene ndidaŵagwira padzanja nkuŵatulutsa ku dziko la Ejipito. Chipangano chimenecho iwo adaphwanya, ngakhale ndinali Mbuye wao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
si monga pangano limene ndinapangana ndi makolo ao tsiku lija ndinawagwira manja kuwatulutsa m'dziko la Ejipito; pangano langa limenelo analiswa, ngakhale ndinali mbuyao, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Silidzakhala ngati pangano limene ndinachita ndi makolo awo pamene ndinawagwira padzanja nʼkuwatulutsa ku Igupto; chifukwa anaphwanya pangano langa, ngakhale ndinali mwamuna wawo,” akutero Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
si monga pangano limene ndinapangana ndi makolo ao tsiku lija ndinawagwira manja kuwaturutsa m'dziko la Aigupto; pangano langa limenelo analiswa, ngakhale ndinali mbuyao, ati Yehova.