Jeremiah 31:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma chipangano chimene ndidzachite ndi anthu a ku Israele atatha masiku amenewo, ndi ichi: Ndidzaika malamulo anga mwa iwo, ndidzachita kuŵalemba m'mitima mwao. Tsono Ineyo ndidzakhala Mulungu wao, ndipo iwowo adzakhala anthu anga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ili ndi pangano limene ndidzapangana ndi nyumba ya Israele atapita masiku aja, ati Yehova; ndidzaika chilamulo changa m'kati mwao, ndipo m'mtima mwao ndidzachilemba; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, nadzakhala iwo anthu anga;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ili ndi pangano limene ndidzachita ndi Aisraeli atapita masiku amenewo,” akutero Yehova. “Ndidzayika lamulo langa mʼmitima mwawo ndi kulilemba mʼmaganizo mwawo. Ine ndidzakhala Mulungu wawo ndipo iwo adzakhala anthu anga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ili ndi pangano limene ndidzapangana ndi nyumba ya Israyeli atapita masiku aja, ati Yehova; ndidzaika cilamulo canga m'kati mwao, ndipo m'mtima mwao ndidzacilemba; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, nadzakhala iwo anthu anga;