Jeremiah 31:35 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akunenanso kuti, “Iye amene amaŵalitsa dzuŵa masana, amene amaŵalitsa mwezi ndi nyenyezi usiku, amene amavundula nyanja kuti mafunde ake achite mkokomo, ndiye amene dzina lake ndi Chauta Wamphamvuzonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova atero, amene apatsa dzuwa kuti liunikire usana, ndi malemba a mwezi ndi a nyenyezi kuti aunikire usiku, amene atonthoza nyanja, pamene mafunde ake agavira; Yehova wa makamu ndi dzina lake:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, Iye amene amakhazikitsa dzuwa kuti liziwala masana, amene amalamula kuti mwezi ndi nyenyezi ziziwala usiku, amene amavundula nyanja kuti mafunde akokome, dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova atero, amene apatsa dzuwa kuti liunikire usana, ndi malemba a mwezi ndi a nyenyezi kuti aunikire usiku, amene atonthoza nyanja, pamene mafunde ace agabvira; Yehova wa makamu ndi dzina lace: