Jeremiah 31:37 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atangopezeka munthu wotha kupima zakumwamba nkufufuza maziko a dziko lapansi, pamenepo Inenso ndidzalitaya fuko lonse la Israele, chifukwa cha zoipa zimene iwo adachita,” akuterotu Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Yehova, Ngati ukhoza kuyesa thambo la kumwamba, ndi kusanthula pansi maziko a dziko, pamenepo ndidzachotsa mbeu zonse za Israele chifukwa cha zonse anazichita, ati Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, “Ndidzataya fuko la Israeli chifukwa cha machimo awo. Ngati patapezeka munthu amene angathe kupima zakuthambo nʼkufufuza maziko a dziko lapansi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Yehova, Ngati ukhoza kuyesa thambo la kumwamba, ndi kusanthula pansi maziko a dziko, pamenepo ndidzacotsa mbeu zonse za Israyeli cifukwa ca zonse anazicita, ati Yehova.