Jeremiah 31:40 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chigwa chonse m'mene amatayiramo mitembo ndi phulusa, ndiponso minda yonse kuyambira ku mtsinje wa Kidroni mpaka ku ngodya ya Chipata cha Kavalo chakuvuma, zonsezo zidzakhala zopatulikira Chauta. Mpakampaka mzinda wa Yerusalemu sudzaonongedwanso kapena kugwetsedwa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chigwa chonse cha mitembo, ndi cha phulusa, ndi minda yonse kufikira kumtsinje wa Kidroni, kufikira kungodya kwa chipata cha akavalo kuloza kum'mawa, ponsepo padzapatulikira Yehova; sipadzazulidwa, sipadzagwetsedwa konse kunthawi zamuyaya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chigwa chonse mʼmene amatayiramo mitembo ndi phulusa, ndiponso minda yonse kuyambira ku Chigwa cha Kidroni mpaka ku ngodya ya Chipata cha Akavalo mbali ya kummawa, adzakhala malo opatulika a Yehova. Mzindawu sadzawuzulanso kapena kuwuwononga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo cigwa conse ca mitembo, ndi ca phulusa, ndi minda yonse: kufikira ku mtsinje wa Kidroni, kufikira kungondya kwa cipata ca akavalo kuloza kum'mawa, ponsepo padzapatulikira Yehova; sipadzazulidwa, sipadzagwetsedwa konse ku nthawi zamuyaya.