Jeremiah 31:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akuti, “Imbani mokweza ndi mosangalala chifukwa cha Yakobe. Fuulani chifukwa cha mtundu wopambana mitundu yonse. Lalikani, tamandani ndi kulengeza kuti, ‘Chauta wapulumutsa anthu ake, wasunga otsala a Israele.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Yehova atero, Imbirani Yakobo ndi kukondwa, fuulirani mtundu woposawo; lalikirani, yamikirani, ndi kuti, Yehova, mupulumutse anthu anu, ndi otsala a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akuti, “Imbani mosangalala chifukwa cha Yakobo, fuwulani chifukwa cha mtundu wopambana mitundu yonse. Matamando anu amveke, ndipo munene kuti, ‘Yehova wapulumutsa anthu ake otsala a Israeli.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Yehova atero, Yimbirirani Yakobo ndi kukondwa, pfuulirani mtundu woposawo; lalikirani, yamikirani, ndi kuti, Yehova, mupulumutse anthu anu, ndi otsala a Israyeli,