Jeremiah 31:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzaŵatulutsa kuchokera ku dziko lakumpoto. Ndidzaŵasonkhanitsa kuchokera ku malekezero a dziko lapansi. Ndidzasonkhanitsa akhungu ndi opunduka, akazi amene ali ndi pakati ndi amene ali pa nthaŵi yao yochira. Chidzakhala chinamtindi cha anthu obwerera kuno.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, ndidzatenga iwo kudziko la kumpoto, ndidzasonkhanitsa iwo ku malekezero a dziko lapansi, pamodzi ndi osaona ndi opunduka mwendo, mkazi amene ali ndi pakati ndi mkazi alinkubala pamodzi; khamu lalikulu lidzabwera kuno.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taonani, ndidzabwera nawo kuchokera ku dziko la kumpoto, ndidzawasonkhanitsa kuchokera ku malekezero a dziko lapansi. Anthu osaona, olumala, amayi oyembekezera ndi amene ali pa nthawi yawo yochira adzabwera nawo pamodzi. Chidzakhala chikhamu cha anthu obwerera kuno.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, ndidzatenga iwo ku dziko la kumpoto, ndidzasonkhanitsa iwo ku malekezero a dziko lapansi, pamodzi ndi osaona ndi opunduka mwendo, mkazi amene ali ndi pakati ndi mkazi alinkubala pamodzi; khamu lalikuru lidzabwera kuno.