Jeremiah 31:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adzabwerera kwao akulira, koma Ine ndidzaŵaperekeza ndi mtima wachifundo. Ndidzaŵatsogolera ku mitsinje yodzaza ndi madzi. Sadzaphunthwa, njira yao idzakhala yosalala kwambiri. Ine ndine bambo wake wa Israele, Efuremu ndi mwana wanga wachisamba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Adzadza ndi kulira, ndipo ndidzawatsogolera ndi mapembedzero, ndidzawayendetsa kumitsinje yamadzi, m'njira yoongoka m'mene sadzaphunthwa, pakuti ndili Atate wake wa Israele, ndipo Efuremu ali mwana wanga woyamba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Adzabwera akulira; koma Ine ndikuwatonthoza mtima, ndidzawaperekeza. Ndidzawatsogolera ku mitsinje yamadzi mʼnjira yosalala mmene sadzapunthwamo. Chifukwa ndine abambo ake a Israeli, ndipo Efereimu ndi mwana wanga woyamba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Adzadza ndi kulira, ndipo ndidzawatsogolera ndi mapembedzero, ndidzawayendetsa ku mitsinje yamadzi, m'njira yoongoka m'mene sadzapunthwa, pakuti ndiri Atate wace wa Israyeli, ndipo Efraimu ali mwana wanga woyamba.