Jeremiah 32:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Makalatawo ndidaŵapereka kwa Baruki mwana wa Neriya, mdzukulu wa Maseiya, pamaso pa Hanamele msuweni wanga, pamaso pa mboni zimene zidaasaina chipanganocho, ndiponso pamaso pa Ayuda onse okhala m'bwalo la alonda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo ndinapereka kalata wogulirayo kwa Baruki mwana wa Neriya, mwana wa Maseiya, pamaso pa Hanamele mwana wa mbale wa atate wanga, ndi pamaso pa mboni zimene zinalemba pa kalata wogulirayo, pamaso pa Ayuda onse okhala m'bwalo la kaidi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinapereka makalatawo kwa Baruki mwana wa Neriya, mdzukulu wa Maseya pamaso pa Hanameli msuweni wanga, pamaso pa mboni zimene zinasayina panganoli ndiponso pamaso pa Ayuda onse okhala mʼbwalo la alonda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo ndinapereka kalata wogulirayo kwa Baruki mwana wa Neriya, mwana wa Maseya, pamaso pa Hanameli mwana wa mbale wa atate wanga, ndi pamaso pa mboni zimene zinalemba pa kalata wogulirayo, pamaso pa Ayuda onse okhala m'bwalo la kaidi.