Jeremiah 32:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, walamula kuti iweyo utenge makalata a umboni wa chipanganoŵa, inai yomata inai yosamata, uŵasunge m'mbiya kuti akhale nthaŵi yaitali.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele atero; Tenga akalata awa, kalata uyu wogulira, wosindikizidwa, ndi kalata uyu wovundukuka, nuwaike m'mbiya yadothi; kuti akhale masiku ambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
‘Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Tenga makalata awa a umboni wapangano, iyi yokhala ndi chizindikiro ndi yopanda chizindikiro, uwasunge mʼmbiya kuti akhale nthawi yayitali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli atero; Tenga akalata awa, kalata uyu wogulira, wosindikizidwa, ndi kalata uyu wobvundukuka, nuwaike m'mbiya yadothi; kuti akhale masiku ambiri.